MULUNGU NDIPONSO CHILENGEDWE - Na

Chichewa

KOSI YOPHUNZITSA BAIBULO YA MA CHRISTADELPHIAN                           Na. 5

 

MULUNGU NDIPONSO CHILENGEDWE

Kuwerenga : Genesis 1; 2:1-7

Chilengedwe

M’chaputala choyambirira m’Baibulo, chomwe ndi Genesis 1, munawerenga zokhudza masiku 7 amene Mulungu analenga zinthu. Tchati chili m’munsimu chikusonyeza zimene zinachitika pa tsiku lililonse pa masiku 7 olenga zinthu:

Tsiku

 

Kunja kunawala; usana ndi usiku zinakhadzikitsidwa

Madzi analekanitsidwa; m’mwamba munaoneka

Mtunda unaoneka. Udzu, zomera ndi mitengo zinalengedwa

Dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zinaoneka

Nsomba zinaoneka m’nyanja; mbalame zinauluka mlengalenga

Nyama zinalengedwa; ndipo chomaliza mwa zonse, Mulungu anapanga mwamuna ndi mkazi

Mulungu anapuma

Onani m’mene chilichonse chikutsatira ndondomeko yake moyenera. Mwachitsanzo, zomera ndi mitengo zinalengedwa pa tsiku lachitatu, pamene mtunda unakhazikitsidwa kuti zomerazo zimerepo. Nyama zinalengedwa tsiku la 7, pamene zakudya zawo (zomera) zinalengedwa kale kuti nyamazo zizidya.

"Ndipo Mulungu anaona chilichonse chimene anapanga, taonani, chinali chabwino."

Tikayang’ana kwina kulikonse, timaona ntchito zodabwitsa zimene Mulungu analenga. Anthu apanga zinthu ngati ndege ndiponso mankhwala a kuchipatala. Koma zimenezi n’zosanunkha kanthu tikaziyerekezera ndi luso komanso mphamvu zimene zinafunika kuti zinthu zonsezi zilengedwe mwadongosolo kwambiri ngati mmene zililimu. Mwachitsanzo, kunja kumada komanso kumacha; pali nyengo zosiyanasiyana zimene zimabwera motsatizanatsatizana, ndipo timadziwa kuti zimenezi zipitirirabe. Zimene anthu amapanga nthawi zina zimawonongeka komanso kulakwika koma zimene Mulungu amachita sizingalakwike.

Zinthu zambiri zimene anthu amapanga zimakhala zonyansa; koma chilichonse chimene Mulungu achita si chimangokwaniritsa cholinga chake moyenera mokha ayi: chimakwaniritsa  mwabwino ndi mochititsa kaso. Kaduwa kakang’ono ka mtengo ndi mphamvu yake yakuti kabereke mtengo wina, ndi chinthu chodabwitsa kwambiri. Chimodzimodzinso kambalame kakang’ono ndi mapiko ake oulukira, ndipo ndi kumatha kuuluka mtunda wautali m’dziko lonse lapansi.

"Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi" (Salmo 8:1)

Milungu yomwe si yoona

Zaka za zapitazi, anthu akhala akuona zodabwitsa za chilengedwe; ndipo m’malo  mopembedza Mulungu amene analenga zinthuzi, akhala akumapembeza zinthu zimene Mulungu analenga! Ngakhale anthu a Mulungu amene,  Ayuda, achitapo izi kwa nthawi zambiri. Anthu akhala akupembeza dzuwa, mwezi ndi nyenyezi; iwo anali kuganiza kuti  zimenezi zinali mizimu imene inali kukhala m’madzi ndi mu mphepo, mu nkhalango ndi m’matanthwe. Ichi ndi chinthu choipa kuchichita, ndipo ndi choletsedwa ndi Mulungu. Tawerengani zimene Paulo anena pa nkhani imeneyi pa Aroma 1: 20-23. Onetsetsani kwenikweni pa vesi 23:

// . . . nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosawonongeka, naufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu wowonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zokwawa."

Zoonadi, pamene anthu anali kupembedza milungu yonama iyi, milunguyo siimatha kuwayankha. Milunguyo ikanayankha bwanji, popeza siinali milungu yeniyeni? Kupembedza milungu yabodza ndi chinthu cholakwika kwambiri, ndipo zoterezi zachititsa anthu kumachita zinthu zoipa; ngakhale zinthu zoipa kwambiri monga kuotcha ana awo pa moto. Chimodzimodzinso Ayuda omwe, ngakhale iwo anapatsidwa malamulo a chilungamo a Mulungu,  analinso kupembedza mafano. Mulungu anawachenjeza iwo pa zinthu ngati izi. Werengani chenjezo lake la Mulungu pa Deuteronomo 4:15-19.

Tsopano taonani pa Ezekieli 14:1-5. Taonani m’mene Mulungu akunenera za anthu awa opembedza mafano pa ndime 3, kuti iwo ‘anautsa mafano awo mumtima mwawo’. Ifenso tikhoza kuchita izi. Ngati pali chinthu china chilichonse m’moyo mwathu chimene timaganiza kuti ndi chofunika kwambiri kuposa Mulungu amene anatilenga, ndiye kuti chinthu chimenechi chikhoza kukhala fano mumtima mwathu.

Ngati tifuna kukondweretsa Mulungu, tiyenera kusakhudzidwa ndi kupembedza mafano. Ndiponso tisakhudzidwe ndi anthu amene apembedza mafano. Paulo akunena  izi pa 2 Akorinto 6:14, pamene akuti:

"Musakhale omangika m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi  chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?"

Ndiyeno werengani nkhaniyi mpaka kumapeto kwa mutu umenewu. Kenaka pitani ku 1 Atesalonika 1: 9,10, pamene tikuuzidwa pomwe Atesalonika “ . . . anatembenukira kwa Mulungu posiyana nawo mafano, kutumikira Mulungu  weniweni wamoyo; ndi kulindilira Mwana wake achokere kumwamba, amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu, wotipulumutsa ife ku mkwiyo ulimkudza.”

Dziko limene anthu aliwononga

Anthu ali kuchita tchimo polambira mafano. Ndipo anthu akuchita tchimo powononga dziko lapansi limene Mulungu analilenga.

Pachiyambi dziko lathu lapansi lino linali malo okongola kwambiri kuposa momwe lilili lero lino. Anthu achita zambiri kuononga kukongola kwa dzikoli. Adula mitengo mosasamala, kubweretsa chipululu m’malo amene munali mitengo yambiri kale. Awononga mpweya ndi utsi woopsa, awononga mitsinje ndi zotsalira popanga zinthu ku mafakitale awo. Mwa izi, ndi njira zina zambiri, dziko lathu lawonongeka.

Koma ngakhale dzikoli lawonongeka chonchi, ndi dziko la Mulungu ndithu. Ndipo Iye sadzalola anthu kuti adzipitirizabe kuliwononga mpaka kalekale. Pa Machitidwe 17:31, mtumwi Paulo akuti,

"Mulungu anapangira tsiku, limene adzaweruza dziko."

Tsiku likubwera pamene Mulungu adzatumizanso Yesu kudzalamulira pano pa dziko. Ulamuliro wake wanzeru ndi malamulo ake achilungamo zidzabwezeretsa dziko kukongola kwake kumene kunalipo pachiyambi. Mulungu wanena kuti, “Koma ndithu pali  Ine, dziko lonse lapansi lidzadzazidwa ndi ulemelero wa Yehova".

Mulungu Wamphamvuyonse

Masalmo 90:2 akuti: “Kuyambira nthawi zosayamba kufikira nthawi zosatha, Inu ndinu Mulungu.” Ichi ndi chimene maganizo athu achigwiritse. Tikudziwa kuchokera pa zomwe taziona m’moyo mwathu  kuti zinthu zonse zili ndi chiyambi ndiponso zili ndi chimaliziro; ndiponso tikudziwa bwino za kubadwa ndi imfa. Koma Ambuye Mulungu akhala alipobe m’mbuyo monsemu ndipo adzakhalapobe m’tsogolo monsemo. Tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro kuti izi zili chonchi chifukwa, monga wolemba kwa Ahebri akuti,

"Koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kum’kondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye" (Ahebri 11:6).

Tikhoza kuyang’ana pa zinthu zodabwitsa za chilengedwe, ndi kuphunzirapo chinthu china pa mphamvu ndi nzeru za Mulungu – koma sitingathe kupeza kuchokera m’dziko lapansi cholinga cha Mulungu polenga dzikoli, kapena zolinga zimene ali nazo pa za dziko lapansi mtsogolo muno. Sitingathe kupeza kuti chifukwa chiyani analenga munthu, kapena chifukwa chiyani Iye akufuna kuti anthuwo akhale ndi moyo.

Kudzera M’mawu Ake Okha tingathe kupeza zinthu zimenezi. Kuti tidziwe zokhudza Mulungu, tiyenera tibwere ku buku lopatulika. Buku lopatulika limatiuza ife kuti Iye ndi wamkulu ndiponso wabwino; limatiuza ife kuti Iye akukonza ndondomeko yokhudza dziko lapansi. Tamverani mawu m’mene Iye akudziulula yekha kwa Mose:

"Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulangira ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate awo, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinayi." (Eksodo 34:6,7).

Mulungu ndi wachifundo ndi wachikondi, ndipo alinso wachilungamo. Iye amayembekezera ife kum’patsa ulemu ndi kumumvera.

Pachiyambi . . .

Anthu ambiri amakhulupilira kuti dziko lathu lapansi lodabwitsali linangokhalapo lokha popanda wolilenga. Iwo amaganiza kuti moyo unangodzibwerera wokha, ndipo kuchokera pa chiyambi chimenechi, zaka zambirimbiri zapitazo, kunangobwera dziko lokongola limene tikuliona leroli. Ndipo amanena kuti zinthu zodabwitsa ngati maso amene timaonera zinthu ndi makutu amene timamvera nawo mawu, zinangokhalako mwamwayi, popanda kulengedwa.

Kenako akatswiri a sayansi anayamba kukhulupirira kuti zinthu zonse za moyo zinachita kusintha kuchokera zinthu zina zopanda moyo. Iwo amati dziko lapansili linabwera chifukwa cha kusinthu kwa zinthu pang’onopang’ono m’zaka zambirimbiri zapitazo. Komabe lero, anthu odziwika ndi ophunzira bwino za sayansi akumabwera ndi maganizo oti zinthu zonse ndi zadongosolo ndipo payenera kuti pali winawake wanzeru amene anapanga zinthu zimenezi, osati zinangokhalako zokha. Baibulo limanena kuti:

"PACHIYAMBI MULUNGU ANALENGA KUMWAMBA NDI DZIKO LAPANSI."

Baibulo silimatiuza mwatsatanetsatane chilichonse chimene Mulungu anachita polenga zinthu chifukwa sitikanatha kuzimvetsa. Ife kwathu ndi kungovomereza mawu ake ndi chikhulupiriro. Chinthu chimodzi chofuna kudziwa ndi ichi – ife sitingathe kukhulupirira chiphunzitso cha buku lopatulika kuti Mulungu analenga zinthu zonse, kenaka ndi kumakhulupiriranso kuti dziko lapansi likangobwera mwadzidzidzi popanda mphamvu ina ili yonse.

"Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova, ndipo ndi mpweya wa m’kamwa mwache khamu lao lonse" (Salmo 33:6).

Mitu yoyamba ya buku la Genesis imatiuza uthenga wofanana ndi umene uli pamwambapo.Tiyenera kumvetsetsa mitu yoyambilira ya buku lopatulika imeneyi isanafike nthawi yakuti timvetsetse ntchito za Ambuye Yesu pogonjetsa tchimo ndi imfa, zimene timawerenga mu Uthenga Wabwino.

Taona m’mutu woyamba wa Genesis m’mene Mulungu analengera dziko lapansi, ndi m’mene analengera mwamuna ndi mkazi pa tsiku lachisanu ndi chimodzi. Tsopano werengani Genesis 2:15 mpaka Genesis 3:24. Ndime zimenezi zimatiuza  nkhani yomvetsa chisoni. Pachiyambi, chilichonse chinali bwino kwambiri m’munda wa Edeni. Kenaka Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu, ndipo kusamvera kwawo kunabweretsa tchimo ndi imfa m’dziko lapansi.

Mwa chikondi chake kwa anthu, patapita zaka zambiri Mulungu anapereka mwana wake, Ambuye Yesu Khristu. Yesu, mwa moyo wake wangwiro ndi imfa yake pa mtanda, anatha kupereka njira kwa Mulungu yokhululukira machimo. Yesu anatibweretsera chiyembekezo cha moyo. Mudzawerenga za nkhaniyi m’phunziro lanu lotsatira.

Anthufe tili m’gulu la zinthu zimene Mulungu analenga

"Tiyeni, tipembedze tiwerame; Tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga" (Salmo 95:6).

Kutha kugwada pamaso pa Mulungu kum’pembedza ndi kumuyamika ndi chinthu chonyaditsa kwambiri. Yesu amanena za anthu amene amabwera kupembedza “mu mzimu ndi mu choonadi”. Iye akuti, “Pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake.” (Yohane 4:23). Mulungu amafuna anthu amene angamukhulupirire ndi kumumvera Iye, ndipo ndi kumasangalala m’dziko limene walenga.

Mulungu amafuna anthu akuti alola kuti Iye aziwatsogolera m’moyo wawo. Iye akukonza anthu oterewa kuti akonzekere nthawi imene iwo adzakhoza kutumikira Mulungu kwa muyaya mu Ufumu wake, pamene Yesu Khristu adzabweranso pano pa dziko lapansi. Ngati tiwerenga mawu ake, ndi kum’lemekeza ndi kumumvera Iye lero, pa tsiku ilo tidzakhala pamodzi ndi amene adzanena,

"Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu, tam’lindilira Iye tidzakondwa ndi kusekerera m’chipulumutso chake" (Yesaya 25:9).

Mwachidule

1. Dziko lapansili linalengedwa ndi Ambuye Mulungu.

2. Iye yekha ndiye woyenera kulambiridwa.

3. Zonse zimene zimanena anthu ophunzira a sayansi za m’mene dzikoli linabwerera ndi zabodza ngati iwo akana kuti Mulungu ndiye mlengi.

4. Tingapeze zambiri zokhuza Mulungu, ndi cholinga chake padziko lapansi, powerenga Baibulo.

5. Baibulo lidzatiphunzitsa ife momwe tingagonjetsere tchimo ndi imfa kupyolera mwa Ambuye Yesu, ndipo tidzagawana nawo za Ufumu wa Mulungu pamene Yesu adzabweranso pano pa dziko lapansi.

Mavesi oyenera kuwerenga :   Salmo 24; Salmo 102:25-28; Aroma 1:18-23;

Genesis 2:15-3:24

Lowezani :   Ahebri 11:3.

Christadelphian Bible Mission Box CBM, 404 Shaftmoor Lane, Birmingham B28 8SZ, England

Swahili Title
Mungu na Uumbaji - Somo la 05
Swahili Word file
PDF file
Hebrew file
Arabic file
English only
D7 Node Id
1252